Salimo 41
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka;
Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.
Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake;
Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko
ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.
Yehova adzamuthandiza pamene akudwala
ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.
 
Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo;
chiritseni pakuti ndakuchimwirani.”
Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti,
“Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?”
Pamene wina abwera kudzandiona,
amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe;
kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja.
 
Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane,
iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti,
“Matenda owopsa amugwira;
sadzaukapo pamalo pamene wagona.”
Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira,
iye amene amadya pamodzi ndi ine
watukula chidendene chake kulimbana nane.
 
10 Koma Yehova mundichititre chifundo,
dzutseni kuti ndiwabwezere.
11 Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane,
pakuti mdani wanga sandigonjetsa.
12 Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga
ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.
 
13 Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli
kuchokera muyaya mpaka muyaya.
Ameni ndi Ameni.