Salimo 68
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;
adani ake athawe pamaso pake.
Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.
Monga phula limasungunukira pa moto,
oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.
Koma olungama asangalale
ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;
iwo akondwere ndi kusangalala.
 
Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,
mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;
dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.
Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,
ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.
Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,
amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;
koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.
 
Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,
pamene munayenda kudutsa chipululu,
dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,
pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.
Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.
Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;
munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.
10 Anthu anu anakhala mʼmenemo
ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.
 
11 Ambuye analengeza mawu,
ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;
12 “Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro;
mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.
13 Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto,
mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva,
nthenga zake ndi golide wonyezimira.”
14 Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko,
zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.
 
15 Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero;
mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.
16 Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri,
pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira,
kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?
17 Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka,
ndi miyandamiyanda;
Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.
18 Pamene Inu munakwera mmwamba,
munatsogolera a mʼndende ambiri;
munalandira mphatso kuchokera kwa anthu,
ngakhale kuchokera kwa owukira,
kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.
 
19 Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu
amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.
20 Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;
Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.
 
21 Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,
zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.
22 Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani;
ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.
23 Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu,
pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”
 
24 Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;
mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.
25 Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;
pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.
26 Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;
tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.
27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,
pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,
ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.
 
28 Kungani mphamvu zanu Mulungu;
tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.
29 Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,
mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.
30 Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,
gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.
Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.
Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.
31 Nthumwi zidzachokera ku Igupto;
Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.
 
32 Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi
imbirani Ambuye matamando.
Sela
33 Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba
amene amabangula ndi mawu amphamvu.
34 Lengezani za mphamvu za Mulungu,
amene ulemerero wake uli pa Israeli
amene mphamvu zake zili mʼmitambo.
35 Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;
Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.
 
Matamando akhale kwa Mulungu!