Salimo 71
Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;
musalole kuti ndichititsidwe manyazi.
Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,
mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.
Mukhale thanthwe langa lothawirapo,
kumene ine nditha kupita nthawi zonse;
lamulani kuti ndipulumuke,
pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.
Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,
kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.
 
Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,
chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.
Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;
Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,
ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.
Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri
koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.
Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,
kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.
 
Musanditaye pamene ndakalamba;
musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.
10 Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;
iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.
11 Iwo amati, “Mulungu wamusiya;
mutsatireni ndi kumugwira,
pakuti palibe amene adzamupulumutse.”
12 Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,
bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.
13 Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,
iwo amene akufuna kundipweteka
avale chitonzo ndi manyazi.
 
14 Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,
ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.
15 Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,
za chipulumutso chanu tsiku lonse,
ngakhale sindikudziwa muyeso wake.
16 Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.
Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.
17 Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,
ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa
18 Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu
musanditaye Inu Mulungu,
mpaka nditalengeza mphamvu zanu
kwa mibado yonse yakutsogolo.
 
19 Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.
Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,
amene mwachita zazikulu?
20 Ngakhale mwandionetsa mavuto
ambiri owawa,
mudzabwezeretsanso moyo wanga;
kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,
mudzandiukitsanso.
21 Inu mudzachulukitsa ulemu wanga
ndi kunditonthozanso.
 
22 Ndidzakutamandani ndi zeze
chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,
ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,
Inu Woyera wa Israeli.
23 Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe
pamene ndidzayimba matamando kwa Inu
amene mwandiwombola.
24 Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo
tsiku lonse,
pakuti iwo amene amafuna kundipweteka
achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.