Salimo 76
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu.
Mulungu amadziwika mu Yuda;
dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.
Tenti yake ili mu Salemu,
malo ake okhalamo mu Ziyoni.
Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka,
zishango ndi malupanga, zida zankhondo.
Sela
 
Wolemekezeka ndinu,
wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.
Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma,
Iwowo amagona tulo tawo totsiriza;
palibe mmodzi wamphamvu
amene angatukule manja ake.
Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo,
kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.
Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa.
Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?
Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo,
ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,
pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze,
kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko.
Sela
10 Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando
ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.
 
11 Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse;
anthu onse omuzungulira abweretse mphatso
kwa Iye amene ayenera kuopedwa.
12 Iye amaswa mzimu wa olamulira;
amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.