Salimo 85
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora.
Yehova munakomera mtima dziko lanu;
munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo.
Munakhululukira mphulupulu za anthu anu
ndi kuphimba machimo awo onse.
Sela
Munayika pambali ukali wanu wonse
ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa.
 
Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.
Kodi mudzatikwiyira mpaka liti?
Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse?
Kodi simudzatitsitsimutsanso,
kuti anthu anu asangalale mwa Inu?
Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova,
ndipo tipatseni chipulumutso chanu.
 
Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena;
Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake,
koma musawalole kuti abwerere ku zopusa.
Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye,
kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.
 
10 Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi;
chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana.
11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi,
ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.
12 Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino,
ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.
13 Wolungama amapita patsogolo pake
ndi kukonza njira za mapazi ake.