Salimo 9
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a nyimbo ya “Imfa ya Mwana.” Salimo la Davide.
Ine ndidzakutamandani, Inu Yehova, ndi mtima wanga wonse;
ndidzafotokoza za zodabwitsa zanu zonse.
Ndidzakondwa ndi kusangalala mwa inu;
Ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina lanu, Inu Wammwambamwamba.
 
Adani anga amathawa,
iwo amapunthwa ndi kuwonongedwa pamaso panu.
Pakuti Inu mwatsimikiza za kulungama kwanga ndi mlandu wanga;
Inu mwakhala pa mpando wanu waufumu, kuweruza mwachilungamo.
Mwadzudzula mitundu ya anthu ndipo mwawononga anthu oyipa;
Inu mwafafaniza dzina lawo kwamuyaya.
Chiwonongeko chosatha chagwera adani,
mwafafaniza mizinda yawo;
ngakhale chikumbutso chawo chawonongedwa.
 
Yehova akulamulira kwamuyaya;
wakhazikitsa mpando wake waufumu woweruzira.
Iye adzaweruza dziko mwachilungamo;
adzalamulira mitundu ya anthu mosakondera.
Yehova ndiye kothawirako kwa opsinjika mtima,
linga pa nthawi ya mavuto.
10 Iwo amene amadziwa dzina lanu adzadalira Inu,
pakuti Inu Yehova, simunawatayepo amene amafunafuna inu.
 
11 Imbani nyimbo zamatamando kwa Yehova, ali pa mpando waufumu mu Ziyoni;
lengezani pakati pa mitundu ya anthu zimene wachita.
12 Pakuti Iye amene amabwezera chilango akupha anzawo wakumbukira;
Iye salekerera kulira kwa ozunzika.
 
13 Inu Yehova, onani momwe adani anga akundizunzira!
Chitireni chifundo ndipo ndichotseni pa zipata za imfa,
14 kuti ndilengeze za matamando anu
pa zipata za ana aakazi a Ziyoni,
kuti pamenepo ndikondwere ndi chipulumutso chanu.
15 Mitundu ya anthu yagwa mʼdzenje limene yakumba;
mapazi awo akodwa mu ukonde umene anawubisa.
16 Yehova amadziwika ndi chilungamo chake;
oyipa akodwa ndi ntchito za manja awo.
Higayoni. Sela
17 Oyipa amabwerera ku manda,
mitundu yonse imene imayiwala Mulungu.
18 Koma osowa sadzayiwalika nthawi zonse,
kapena chiyembekezo cha ozunzika kutayika nthawi zonse.
 
19 Dzukani Inu Yehova, musalole munthu kuti apambane;
mitundu yonse iweruzidwe pamaso panu.
20 Akantheni ndi mantha aakulu, Inu Yehova;
mitundu idziwe kuti iwo ndi anthu wamba.
Sela