1 Mbiri
1
Mbiri ya Makolo Kuchokera pa Adamu Mpaka pa Abrahamu
Mpaka pa Ana a Nowa
1 Adamu, Seti, Enosi
2 Kenani, Mahalaleli, Yaredi,
3 Enoki, Metusela, Lameki, Nowa.
4 Ana a Nowa,
Semu, Hamu ndi Yafeti.
Fuko la Yafeti
5 Ana aamuna a Yafeti anali:
Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi.
6 Ana aamuna a Gomeri anali:
Asikenazi, Rifati ndi Togarima
7 Ana aamuna a Yavani anali:
Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu.
Fuko la Hamu
8 Ana aamuna a Hamu anali:
Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani
9 Ana aamuna a Kusi anali:
Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka
Ana aamuna a Raama anali:
Seba ndi Dedani.
10 Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu
kwambiri pa dziko lapansi.
11 Igupto ndiye kholo la
Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu,
12 Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori.
13 Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni,
ndipo anaberekanso Ahiti,
14 Ayebusi, Aamori, Agirigasi
15 Ahivi, Aariki, Asini
16 Aaravadi, Azemari ndi Ahamati.
Fuko la Semu
17 Ana aamuna a Semu anali:
Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu.
Ana aamuna a Aramu anali:
Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki.
18 Aripakisadi anabereka Sela
ndipo Selayo anabereka Eberi:
19 Eberi anabereka ana aamuna awiri:
wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani.
20 Yokitani anabereka
Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera,
21 Hadoramu, Uzali, Dikila
22 Obali, Abimaeli, Seba,
23 Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani.
24 Semu, Aripakisadi, Sela
25 Eberi, Pelegi, Reu
26 Serugi, Nahori, Tera
27 ndi Abramu (amene ndi Abrahamu).
Banja la Abrahamu
28 Ana a Abrahamu ndi awa:
Isake ndi Ismaeli.
Zidzukulu za Hagara
29 Zidzukulu zake zinali izi:
Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu,
30 Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema,
31 Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli.
Zidzukulu za Ketura
32 Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa:
Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa.
Ana a Yokisani ndi awa:
Seba ndi Dedani
33 Ana aamuna a Midiyani anali,
Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida.
Onsewa anali zidzukulu za Ketura.
Zidzukulu za Sara
34 Abrahamu anabereka Isake.
Ana a Isake anali awa:
Esau ndi Israeli.
Ana a Esau
35 Ana aamuna a Esau anali awa:
Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora.
36 Ana a Elifazi anali awa:
Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi:
Amene anabereka ndi Timna: Amaleki.
37 Ana a Reueli anali awa:
Nahati, Zera, Sama ndi Miza.
Anthu a ku Seiri ku Edomu
38 Ana a Seiri anali awa:
Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani.
39 Ana aamuna a Lotani anali awa:
Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani.
40 Ana aamuna a Sobala anali awa:
Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu.
Ana aamuna a Zibeoni anali awa:
Ayiwa ndi Ana.
41 Mwana wa Ana anali
Disoni.
Ana a Disoni anali awa:
Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani
42 Ana aamuna a Ezeri anali awa:
Bilihani, Zaavani ndi Yaakani.
Ana aamuna a Disani anali awa:
Uzi ndi Arani.
Mafumu a ku Edomu
43 Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko:
Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba.
44 Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake.
45 Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake.
46 Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti.
47 Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake.
48 Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake.
49 Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake.
50 Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu.
51 Hadadi anamwaliranso.
Mafumu a ku Edomu anali:
Timna, Aliva, Yeteti,
52 Oholibama, Ela, Pinoni,
53 Kenazi, Temani, Mibezari,
54 Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu.