17
Lonjezo la Mulungu kwa Davide
1 Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.”
2 Natani anayankha Davide kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu, chifukwa Mulungu ali nanu.”
3 Usiku umenewo mawu a Mulungu anafika kwa Natani, ndipo anati,
4 “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’
5 Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Israeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda kuchoka mʼtenti ina kupita mʼtenti ina, kuchoka malo ena kupita malo ena.
6 Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ”
7 Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli.
8 Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi.
9 Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja;
10 monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzagonjetsanso adani anu onse.
“ ‘Ine ndikulengeza kwa iwe kuti Yehova adzakhazikitsa banja lako.
11 Masiku ako akadzatha ndipo ukadzatsatira makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, mmodzi mwa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake.
12 Iye ndiye amene adzandimangira nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya.
13 Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo.
14 Ndidzamuyika kukhala wolamulira nyumba yanga ndi ufumu wanga kwamuyaya. Mpando wake waufumu udzakhazikika kwamuyaya.’ ”
15 Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira.
Pemphero la Davide
16 Choncho Mfumu Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati,
“Ine ndine yani, Inu Yehova Mulungu, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?
17 Inu Mulungu, kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inuyo mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Mwandiyangʼana ndipo mwandiyesa ngati munthu wolemekezeka kwambiri pakati pa anthu, Inu Yehova Mulungu.”
18 “Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu, pakuti mwachitira ulemu wotere mtumiki wanu? Pakuti Inu mukumudziwa mtumiki wanu.
19 Inu Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwawulula malonjezo anu aakulu onse.
20 “Palibe wina wofanana nanu, Inu Yehova, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha monga tamvera ndi makutu athu.
21 Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto?
22 Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.
23 “Ndipo tsopano Yehova, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake, likhazikitseni kwamuyaya. Chitani monga mwalonjezera,
24 kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
25 “Inu Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzamumangira nyumba. Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere.
26 Inu Yehova, ndinu Mulungu! Mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu.
27 Ndipo chakukomerani kudalitsa banja la mtumiki wanu kuti likhale pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti Inu Yehova mwalidalitsa, lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”