23
Fuko la Levi
1 Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli.
2 Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi.
3 Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000.
4 Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza.
5 Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.”
6 Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari.
Banja la Geresoni
7 Ana a Geresoni:
Ladani ndi Simei.
8 Ana a Ladani:
Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu.
9 Ana a Simei:
Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu.
Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani.
10 Ndipo ana a Simei anali:
Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya.
Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi.
11 Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana.
Banja la Kohati
12 Ana a Kohati:
Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi.
13 Ana a Amramu:
Aaroni ndi Mose.
Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya.
14 Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi.
15 Ana a Mose:
Geresomu ndi Eliezara.
16 Zidzukulu za Geresomu:
Mtsogoleri anali Subaeli.
17 Zidzukulu za Eliezara:
Mtsogoleri anali Rehabiya.
Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri.
18 Ana a Izihari:
Mtsogoleri anali Selomiti.
19 Ana a Hebroni:
Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi.
20 Ana a Uzieli:
Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya.
Banja la Merari
21 Ana a Merari:
Mahili ndi Musi.
Ana a Mahili:
Eliezara ndi Kisi.
22 Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira.
23 Ana a Musi:
Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu.
24 Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova.
25 Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya,
26 sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.”
27 Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo.
28 Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu.
29 Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake.
30 Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo,
31 ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira.
32 Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova.