26
Alonda a pa Zipata
1 Magulu a alonda a pa zipata:
Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu.
2 Meselemiya anali ndi ana awa:
woyamba Zekariya,
wachiwiri Yediaeli,
wachitatu Zebadiya,
wachinayi Yatinieli,
3 wachisanu Elamu,
wachisanu ndi chimodzi Yehohanani,
ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai.
4 Obedi-Edomu analinso ndi ana awa:
woyamba Semaya,
wachiwiri Yehozabadi,
wachitatu Yowa,
wachinayi Sakara,
wachisanu Netaneli,
5 wachisanu ndi chimodzi Amieli,
wachisanu ndi chiwiri Isakara
ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi.
(Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu).
6 Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu.
7 Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu.
8 Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62.
9 Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18.
10 Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri),
11 wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13.
12 Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo.
13 Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse.
14 Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye.
15 Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake.
16 Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa.
Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake:
17 Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu.
18 Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni.
19 Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari.
Asungichuma ndi Akuluakulu Ena
20 Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu.
21 Adzukulu a Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, amene anali atsogoleri a mabanja a Ageresoni, anali awa: Yehieli,
22 ana a Yehieli, Zetamu ndi mʼbale wake Yoweli. Iwo amayangʼanira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu wa Yehova.
23 Kuchokera ku banja la Amramu, banja la Aizihara, banja la Ahebroni ndi banja la Auzieli:
24 Subaeli, chidzukulu cha Geresomu, mwana wa Mose, anali mkulu woyangʼanira chuma.
25 Abale ake obadwa mwa Eliezara, anali Rekabiya mwana wake, Yesaya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake ndi Selomiti mwana wake.
26 Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena.
27 Zina zofunkha ku nkhondo anazipereka kuti zikhale zokonzera Nyumba ya Yehova.
28 Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake.
29 Kuchokera ku banja la Izihari: Kenaniya ndi ana ake anapatsidwa ntchito kutali ndi Nyumba ya Mulungu ngati akuluakulu ndi oweruza Israeli.
30 Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani.
31 Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi.
32 Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu.