7
Fuko la Isakara
1 Ana a Isakara anali awa:
Tola, Puwa, Yasubu ndi Simironi ndipo onse analipo anayi.
2 Ana a Tola ndi awa:
Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600.
3 Mwana wa Uzi anali
Izirahiya.
Ana a Izirahiya anali:
Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse asanu anali atsogoleri a mabanja.
4 Monga mwa chiwerengero cha mabanja awo, panali anthu 36,000 odziwa kumenya nkhondo, pakuti iwo anali ndi akazi ndi ana ambiri.
5 Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo.
Fuko la Benjamini
6 Ana atatu a Benjamini anali awa:
Bela, Bekeri ndi Yediaeli.
7 Ana a Bela anali awa:
Eziboni, Uzi, Uzieli, Yerimoti ndi Iri. Iwowa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo onse pamodzi analipo asanu. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali anthu 22,034 odziwa kumenya nkhondo.
8 Ana a Bekeri anali awa:
Zemira, Yowasi, Eliezara, Eliyoenai, Omiri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri.
9 Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali atsogoleri a mabanja ndi anthu 20,200 odziwa kumenya nkhondo.
10 Mwana wa Yediaeli anali
Bilihani.
Ana a Bilihani anali awa:
Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara.
11 Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo.
12 Asupi ndi Ahupi anali zidzukulu za Iri, ndipo Ahusimu anali zidzukulu za Aheri.
Fuko la Nafutali
13 Ana a Nafutali anali awa:
Yahazieli, Guni, Yezeri ndi Salumu, zidzukulu za Biliha.
Fuko la Manase
14 Ana a Manase anali awa:
Asirieli ndi mwana amene anabereka kwa mzikazi wake wa ku Aramu. Mzikazi yemweyo anaberekanso Makiri abambo ake a Giliyadi.
15 Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka.
Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha.
16 Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Perezi. Mʼbale wake anamutcha Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rakemu.
17 Mwana wa Ulamu anali
Bedani.
Awa anali ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase.
18 Mlongo wake Hamoleketi anabereka Isihodi, Abiezeri ndi Mahila.
19 Ana a Semida anali:
Ahiyani, Sekemu, Likihi ndi Aniyamu.
Fuko la Efereimu
20 Ana a Efereimu anali awa:
Sutela, Beredi,
Tahati, Eliada,
Tahati,
21 Zabadi,
Sutela.
Ezeri ndi Eladi anaphedwa ndi anthu a ku Gati, pamene anabwera kudzalanda zoweta zawo.
22 Efereimu, abambo awo, anawalira masiku ambiri, ndipo abale ake anabwera kudzamutonthoza.
23 Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake.
24 Mwana wake wamkazi anali Seera, amene anamanga mzinda wa Beti-Horoni Wakumunsi, Wakumtunda kudzanso Uzeni-Seera.
25 Mwana wina wa Efereimu anali Refa amene zidzukulu zake zinali Resefu,
Tela, Tahani,
26 Ladani, Amihudi,
Elisama,
27 Nuni
ndi Yoswa.
28 Malo amene ankakhala anali Beteli ndi midzi yozungulira, cha kummawa kunali Naarani, Gezeri ndi midzi yake ya kumadzulo ndi Sekemu ndi midzi yake mpaka ku Aya ndi midzi yake.
29 Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi.
Fuko la Aseri
30 Ana a Aseri anali awa:
Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya. Mlongo wawo anali Sera.
31 Ana a Beriya anali awa:
Heberi ndi Malikieli amene anabereka Birizaiti.
32 Heberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Suwa, mlongo wawo.
33 Ana a Yafuleti anali awa:
Pasaki, Bimuhali ndi Asivati.
Awa anali ana a Yafuleti.
34 Ana a Someri anali awa:
Ahi, Rohiga, Yehuba ndi Aramu.
35 Ana a mʼbale wake Helemu anali awa:
Zofa, Imuna, Selesi ndi Amali.
36 Ana a Zofa anali awa:
Suwa, Harineferi, Suwali, Beri, Imula,
37 Bezeri, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Bera.
38 Ana a Yeteri anali awa:
Yefune, Pisipa ndi Ara.
39 Ana a Ula anali awa:
Ara, Hanieli ndi Riziya.
40 Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000.