18
Mikaya Anenera Motsutsa Ahabu
1 Tsono Yehosafati anali ndi chuma chambiri ndi ulemu, ndipo iye anachita mgwirizano wa ukwati ndi Ahabu.
2 Patapita zaka zina, iye anapita kukacheza kwa Ahabu mu Samariya. Ahabu anaphera iye pamodzi ndi anthu amene anali naye, nkhosa zambiri ndi ngʼombe ndipo anamuwumiriza kuti akathire nawo nkhondo Ramoti Giliyadi
3 Ahabu mfumu ya Israeli anafunsa Yehosafati mfumu ya Yuda kuti, “Kodi mudzapita nane kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi?”
Yehosafati anayankha kuti, “Ine ndili ngati inu nomwe, ndi anthu anga ngati anthu anu. Ife tikhala nanu limodzi pa nkhondoyi.”
4 Koma Yehosafati anatinso kwa mfumu ya Israeli, “Choyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”
5 Tsono mfumu ya Israeli inasonkhanitsa aneneri 400 ndipo inawafunsa kuti, “Kodi tipite kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?”
Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Mulungu adzawupereka mʼdzanja la mfumu.”
6 Koma Yehosafati anafunsanso kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wina wa Yehova amene ife tingafunsireko?”
7 Mfumu ya Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife kudzera mwa iye titha kufunsira kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa sandilosera zabwino koma zoyipa nthawi zonse. Iyeyu ndi Mikaya mwana wa Imula.”
Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu isanene motero.”
8 Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa akuluakulu ake ndipo inati, “Kamutengeni Mikaya mwana wa Imula, abwere msanga.”
9 Mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda, atavala mikanjo yawo yaufumu anali atakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopunthira tirigu pa khomo la chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo.
10 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo ndipo analengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi udzagunda Aaramu mpaka atawonongedwa!’ ”
11 Aneneri ena onse amanenera chimodzimodzi kuti, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo kapambaneni, pakuti Mulungu adzamupereka mʼdzanja la mfumu.”
12 Wauthenga amene anapita kukayitana Mikaya anati kwa iye, “Taonani aneneri ena onse ngati munthu mmodzi akulosera za chipambano cha mfumu. Mawu anunso agwirizane ndi awo ndipo muyankhule zabwino.”
13 Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndidzanena zimene Mulungu wanga andiwuze.”
14 Iye atafika mfumu inamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite ku nkhondo kukalimbana ndi Ramoti Giliyadi kapena tileke?”
Iye anayankha kuti, “Kathireni nkhondo ndipo kapambaneni, pakuti mzindawo udzaperekedwa mʼdzanja lanu.”
15 Mfumu inati kwa iye, “Kodi ndikuwuze kangati kuti ulumbire kuti usandiwuze chilichonse koma zoonadi mʼdzina la Yehova?”
16 Ndipo Mikaya anayankha kuti, “Ine ndinaona Aisraeli atabalalika mʼmapiri monga nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mu mtendere!’ ”
17 Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti sandinenera zabwino koma zoyipa zokhazokha?”
18 Mikaya anapitiriza ndi kunena kuti, “Imvani tsono mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu ndi gulu lonse lakumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi lamanzere.
19 Ndipo Yehova anati, ‘Ndani amene adzamunyengerere Ahabu mfumu ya Israeli kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi ndi kukafera komweko?’
“Wina ananena zina, winanso ananena zina.”
20 Pomaliza mzimu wina unatuluka ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, “Ine ndikamunyengerera!”
Yehova anafunsa kuti, “Ukagwiritsa ntchito njira yanji?”
21 Mzimuwo unati, “Ine ndidzapita ndi kukhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse!”
Yehova anati, “ ‘Iwe ukamunyengadi iyeyo. Pita kachite zimenezo.’
22 “Choncho Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anuwa. Yehova waneneratu kuti inu mukaona tsoka.”
23 Ndipo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi ndi kumenya khofi Mikaya. Zedekiya anafunsa kuti, “Kodi mzimu wochokera kwa Yehova unadzera njira iti pamene unachoka kwa ine kupita kwa iwe?”
24 Mikaya anayankha kuti, “Udzadziwa pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”
25 Pamenepo mfumu ya Israeli inalamula kuti, “Tengani Mikaya ndipo mupite naye kwa Amoni, wolamulira mzindawo ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu,
26 ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyike munthu uyu mʼndende ndipo musamupatse kanthu kalikonse koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwera mwamtendere.’ ”
27 Mikaya anayankhula kuti, “Ngati inu mukabwera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo anawonjeza kuti, “Anthu nonsenu, mumve zimene ndanenazi.”
Ahabu Aphedwa ku Ramoti-Giliyadi
28 Choncho mfumu ya Israeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi.
29 Mfumu ya Israeli inati kwa Yehosafati, “Ine ndipita ku nkhondo modzibisa koma iwe uvale mikanjo yaufumu.” Kotero mfumu ya Israeli inadzibisa ndipo inapita ku nkhondoko.
30 Tsono mfumu ya Aramu inalamulira olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu koma mfumu ya Israeli yokha.”
31 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, iwo anaganiza kuti, “Mfumu ya Israeli ndi iyi.” Kotero anatembenuka kukamenyana naye koma Yehosafati anafuwula, ndipo Yehova anamuthandiza. Mulungu anawabweza mʼmbuyo,
32 pakuti olamulira magaleta ataona kuti sanali mfumu ya Israeli, anasiya kumuthamangitsa.
33 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndipo analasa mfumu ya Israeli pakati polumikizira malaya achitsulo. Mfumu inawuza oyendetsa galeta kuti, “Bwerera, undichotse pa nkhondo pano. Ndavulazidwa.”
34 Nkhondo inakula kwambiri tsiku lonse, ndipo mfumu ya Israeli inakhala tsonga mʼgaleta lake kuyangʼanana ndi Aaramu mpaka madzulo. Ndipo pamene dzuwa linkalowa inamwalira.