8
Moyo Watsopano mwa Khristu
1 Choncho, tsopano amene ali mwa Khristu Yesu alibe mlandu owatsutsa
2 chifukwa mwa Khristu Yesu, lamulo la Mzimu Woyera amene amapereka moyo, lawamasula ku lamulo la tchimo ndi la imfa.
3 Pakuti zimene Malamulo sanathe kuzichita, popeza anali ofowoka chifukwa cha khalidwe lathu la uchimo, Mulungu anazichita potumiza Mwana wake mʼchifanizo cha munthu ochimwa kuti akhale nsembe yauchimo. Ndipo Iye anagonjetsa tchimo mʼthupi la munthu,
4 ndi cholinga chakuti chilungamo chofunikira cha lamulo chikwaniritsidwe kwathunthu mwa ife amene sitikhala monga mwachikhalidwe chathu cha uchimo koma mwa Mzimu.
5 Pakuti anthu amene amakhala monga mwa makhalidwe oyipa a thupi amayika malingaliro awo pa zinthu zathupi. Koma amene amakhala monga mwa Mzimu amayika malingaliro awo pa zinthu za Mzimu.
6 Kuyika mtima pa zathupi ndi imfa koma kuyika mtima pa za Mzimu ndi moyo ndi mtendere.
7 Pakuti mtima umene wakhazikika pa zathupi ndi wodana ndi Mulungu. Sunagonjere lamulo la Mulungu ndipo sungathe kutero.
8 Ndipo anthu amene amalamulidwa ndi khalidwe lauchimo sangathe kukondweretsa Mulungu.
9 Koma inu simulamulidwanso ndi khalidwe lanu lauchimo koma ndi Mzimu ngati Mzimu wa Mulungu akhaladi mwa inu. Koma ngati munthu aliyense alibe Mzimu wa Khristu, iyeyu si wa Khristu.
10 Ndipo ngati Khristu ali mwa inu, thupi lanu ndi lakufa chifukwa cha uchimo, koma mzimu wanu ndi wamoyo chifukwa cha chilungamo.
11 Ndipo ngati Mzimu wa Mulungu amene anaukitsa Yesu kwa akufa akhala mwa inu, Iyeyo amene anaukitsa Khristu kwa akufa adzapatsanso moyo matupi anu amene amafa kudzera mwa Mzimu wake amene amakhala mwa inu.
12 Kotero abale, ife tili ndi zoti tikwaniritse, koma osati za khalidwe lathu lauchimo, kumachita zofuna zake.
13 Pakuti ngati inu mukhala monga mwa khalidwe lauchimo, mudzafa. Koma ngati mwa Mzimu mupha ntchito zoyipa zathupi, mudzakhala ndi moyo.
14 Onse amene amatsogozedwa ndi Mzimu wa Mulungu ndi ana a Mulungu.
15 Mzimu amene inu munalandira samakusandutsani akapolo, kuti muzikhalanso amantha, koma Mzimu amakusandutsani ana. Ndipo mwa Iye ife timafuwula kuti, “Abba, Atate.”
16 Mzimu mwini amavomerezana ndi mzimu wathu kuti ife ndife ana a Mulungu.
17 Tsono ngati tili ana ake, ndiye kuti ndife olowa mʼmalo a Mulungu ndi olowa mʼmalo pamodzi ndi Khristu. Ngati ife timva zowawa pamodzi ndi Khristu, tidzalandiranso ndi ulemerero womwe pamodzi naye.
Ulemerero wa Mʼtsogolo
18 Ine ndiganiza kuti masautso amene tikuwamva nthawi ino, sakufanana ndi ulemerero umene udzaonetsedwa mwa ife.
19 Pakuti chilengedwe chikudikira ndi chiyembekezo kuonetsedwa poyera kwa ana a Mulungu.
20 Pakuti chilengedwe sichinasankhe kugonjera zopanda pake, koma mwachifuniro cha Iye amene analola kuti chigonjere. Koma chili ndi chiyembekezo
21 chakuti chidzamasulidwa ku ukapolo wa chivundi ndi kulandiranso ufulu ndi ulemerero wa ana a Mulungu.
22 Ife tikudziwa kuti chilengedwe chonse chakhala chikubuwula ndi ululu ngati ululu wa nthawi yobereka mwana mpaka tsopano lino.
23 Si zokhazo ayi, ngakhale ife tomwe, amene tili ndi zipatso zoyamba za Mzimu, tikubuwulira mʼkati mwathu pomwe tikudikira mwachidwi kusankhidwa kwathu ngati ana, kuwomboledwa kwa matupi athu.
24 Pakuti ife tinapulumutsidwa mʼchiyembekezo ichi. Koma chiyembekezo chimene chimaoneka si chiyembekezo ayi. Kodi ndani amene amayembekezera chimene ali nacho kale?
25 Koma ngati ife tiyembekeza chimene tikanalibe, ndiye kuti tikuyembekeza modekha mtima.
26 Momwemonso, Mzimu amatithandiza ife mʼkufowoka kwathu. Ife sitidziwa momwe tiyenera kupempherera koma Mzimu mwini amatipempherera mobuwula ndi mawu osafotokozedwa.
27 Koma Iye amene amasanthula mitima yathu amadziwa maganizo a Mzimu, chifukwa Mzimu amapempherera oyera mtima molingana ndi chifuniro cha Mulungu.
Oposa Agonjetsi
28 Ndipo ife tikudziwa kuti zinthu zonse zimathandizana kuwachitira ubwino amene amakonda Mulungu, amene anayitanidwa monga mwa cholinga chake.
29 Pakuti amene Mulungu anawadziwiratu, anawasankhiratunso kuti akonzedwe mʼchifanizo cha Mwana wake, kuti Iye akhale Mwana woyamba kubadwa mwa abale ambiri.
30 Iwo amene anawasankhiratu, anawayitananso. Amene Iye anawayitana anawalungamitsanso ndipo amene anawalungamitsa anawapatsanso ulemerero.
31 Nanga tsono tidzanena chiyani pa izi? Ngati Mulungu ali mbali yathu, adzatitsutsa ife ndani?
32 Iye amene sanatimane Mwana wake wa Iye yekha, koma anamupereka chifukwa cha ife tonse. Iye adzalekeranjinso pamodzi naye kutipatsa ife zinthu zonse mwaulere?
33 Ndani amene adzabweretsa mlandu kutsutsa amene Mulungu anawasankha? Ndi Mulungu amene amalungamitsa.
34 Ndani amene angatipeze ife olakwa? Palibe. Khristu Yesu amene anafa, kuposera pamenepo, amene anaukitsidwa ndi moyo, amene ali kudzanja lamanja la Mulungu ndiye amene akutipempherera.
35 Ndani amene adzatilekanitsa ife ndi chikondi cha Khristu? Kodi ndi masautso, kapena zowawa, kapena mazunzo, kapena njala, kapena umaliseche, kapena choopsa, kapena lupanga?
36 Monga kwalembedwa:
“Chifukwa cha inu, ife tikuphedwa tsiku lonse:
ife tikutengedwa ngati nkhosa zoti zikaphedwe.”
37 Ayi, mu zonsezi ife ndife oposa agonjetsi mwa Iye amene anatikonda.
38 Pakuti ine ndatsimikiza ndi mtima wonse kuti ngakhale imfa, kapena moyo, ngakhale angelo, kapena ziwanda, ngakhale zinthu zilipo, kapena zili mʼtsogolo, kapena mphamvu zina,
39 ngakhale kutalika, kapena kuya, kapena chilichonse mʼchilengedwe chonse, sizingathe kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye athu.