8
Kutsekulidwa kwa Chimatiro Chachisanu ndi Chiwiri
1 Atatsekula chomatira chachisanu ndi chiwiri, kumwamba kunakhala chete mphindi makumi atatu.
2 Ndipo ndinaona angelo asanu ndi awiri aja amene amayimirira pamaso pa Mulungu, akupatsidwa malipenga asanu ndi awiri.
3 Mngelo wina amene anali ndi chofukizira chagolide anabwera nayimirira pa guwa lansembe. Anapatsidwa lubani wambiri kuti amupereke pamodzi ndi mapemphero a anthu onse oyera mtima pa guwa lansembe lagolide patsogolo pa mpando waufumu.
4 Fungo la lubani pamodzi ndi mapemphero a oyera mtima zinakwera kumwamba kwa Mulungu kuchokera mʼdzanja la mngeloyo.
5 Kenaka mngeloyo anatenga chofukizira nachidzaza ndi moto wochokera pa guwa lansembe ndi kuponya pa dziko lapansi ndipo nthawi yomweyo panachitika mabingu, phokoso, mphenzi ndi chivomerezi.
Malipenga
6 Angelo asanu ndi awiri anakonzekera kuyimba malipenga asanu ndi awiri.
7 Mngelo woyamba anayimba lipenga lake ndipo kunabwera matalala ndi moto wosakanizana ndi magazi ndipo unaponyedwa pa dziko lapansi. Gawo limodzi la magawo atatu a dziko lapansi linapsa, gawo limodzi la magawo atatu a mitengo linapsa ndi gawo limodzi la magawo atatu a udzu wauwisi linapsanso.
8 Mngelo wachiwiri anayimba lipenga lake, ndipo chinthu china chooneka ngati phiri lalikulu loyaka moto, chinaponyedwa mʼnyanja. Gawo limodzi la magawo atatu a nyanja linasanduka magazi.
9 Gawo limodzi mwa magawo atatu a zolengedwa zonse zamoyo za mʼnyanja, linafa, ndipo gawo limodzi la sitima za pamadzi linawonongedwa.
10 Mngelo wachitatu anayimba lipenga lake, ndipo nyenyezi yayikulu, yoyaka ngati muni inachoka kumwamba nigwera pa gawo limodzi la magawo atatu a mitsinje ndi pa akasupe amadzi.
11 Dzina la nyenyeziyo ndi Chowawa. Gawo limodzi la magawo atatu a madzi anasanduka owawa ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha madzi owawawo.
12 Mngelo wachinayi anayimba lipenga lake, ndipo chimodzi cha zigawo zitatu za dzuwa, za mwezi ndi za nyenyezi zinamenyedwa kotero chimodzi mwa zitatu za zonsezi zinada. Panalibenso kuwala pa chimodzi mwa zigawo zitatu za usana, ndi chimodzimodzinso usiku.
13 Ndinayangʼananso ndipo ndinaona ndi kumva chiwombankhanga chimene chinkawuluka mlengalenga kwambiri chikuyankhula mofuwula kuti, “Tsoka, Tsoka! Tsoka lalikulu kwa anthu okhala mʼdziko lapansi, angelo otsala aja akangoyimba malipenga awo!”