KALATA YOYAMBA YA PAULO YOLEMBERA
TIMOTEYO
1
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu.
2 Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro.
Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe.
Kutsutsa Aphunzitsi Onyenga
3 Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga,
4 kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro.
5 Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona.
6 Anthu ena anapatuka pa zimenezi ndipo anatsata nkhani zopanda tanthauzo.
7 Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza.
8 Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino.
9 Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena.
10 Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona.
11 Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa.
Chisomo cha Ambuye kwa Paulo
12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake.
13 Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro.
14 Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu.
15 Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa.
16 Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha.
17 Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni.
Ntchito ya Timoteyo
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo
19 utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka.
20 Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu.