13
Kuyeretsedwa ku Tchimo
1 “Pa tsiku limenelo nyumba ya Davide adzayitsekulira kasupe wa madzi pamodzi ndi okhala mu Yerusalemu, kuti awachotsere tchimo lawo ndi chodetsa chawo.
2 “Pa tsiku limenelo, ndidzafafaniziratu mayina a mafano mʼdziko, ndipo sadzawakumbukiranso,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Ndidzachotsa mʼdziko aneneri pamodzi ndi mzimu wonyansa.
3 Ndipo ngati wina aliyense adzafuna kunenera, abambo ndi amayi ake amene anamubereka, adzamuwuza kuti, ‘Uyenera kufa, chifukwa wayankhula bodza mʼdzina la Yehova.’ Pamene anenera, makolo ake omwe adzamubaya.
4 “Pa tsiku limenelo mneneri aliyense adzachita manyazi chifukwa cha masomphenya ake. Sadzavala chovala chake chaubweya ndi cholinga chonamiza anthu.
5 Iye adzati, ‘Sindine mneneri. Ndine mlimi; ndakhala ndi kulima munda kuyambira ubwana wanga.’
6 Ngati wina adzamufunsa, ‘Zilonda zili mʼthupi lakoli ndi chiyani?’ Iye adzayankha kuti, ‘Zilondazi ndinazilandira mʼnyumba ya abwenzi anga.’
Kukantha Mʼbusa, Nkhosa Kubalalika
7 “Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga,
ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Kantha mʼbusa
ndipo nkhosa zidzabalalika,
ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono.
8 Mʼdziko monse, akutero Yehova Wamphamvuzonse,
“zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za anthu zidzakanthidwa ndi kuwonongeka;
koma chigawo chimodzi chidzatsala mʼdzikomo.
9 Chigawo chachitatuchi ndidzachiyika pa moto;
ndidzawayeretsa monga momwe amayeretsera siliva
ndi kuwayesa monga momwe amayesera golide.
Adzayitana pa dzina langa
ndipo Ine ndidzawayankha;
Ine ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’
ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndiye Mulungu wathu.’ ”