6
Magaleta Anayi
1 Ndinayangʼananso ndipo taonani ndinaona magaleta anayi akutuluka pakati pa mapiri awiri, mapiri amkuwa.
2 Galeta loyamba limakokedwa ndi akavalo ofiira, lachiwiri ndi akavalo akuda,
3 lachitatu ndi akavalo oyera, ndipo lachinayi ndi akavalo otuwa a mawanga ofiirira, onsewa anali akavalo amphamvu kwambiri.
4 Ndinafunsa mngelo amene amayankhula nane uja kuti, “Kodi mbuye wanga chimenechi nʼchiyani?”
5 Mngeloyo anandiyankha kuti, “Imeneyi ndi mizimu inayi yakumwamba, imene ikuchokera pamaso pa Ambuye wa dziko lonse.
6 Galeta la akavalo akuda likupita ku dziko la kumpoto, galeta la akavalo oyera likutsatira, ndipo galeta la akavalo amawanga ofiirira likupita ku dziko la kummwera.”
7 Pamene akavalo amphamvuwa ankapita, anali ndi changu chofuna kuyendera dziko lapansi. Ndipo iye anati, “Pitani, kayendereni dziko lapansi!”
8 Pamenepo anandiyitana, “Taona, akavalo amene apita ku dziko la kumpoto apumulitsa Mzimu wanga kumeneko.”
Chipewa Chaufumu cha Yoswa
9 Yehova anayankhula nane kuti,
10 “Landira mphatso kuchokera kwa anthu amene abwera ku ukapolo, Helidai, Tobiya ndi Yedaya, amene achokera ku Babuloni. Tsiku lomwelo pita ku nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya.
11 Tenga siliva ndi golide upange chipewa chaufumu, ndipo uchiyike pamutu pa mkulu wa ansembe, Yoswa mwana wa Yehozadaki.
12 Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova.
13 Ndiye amene adzamange Nyumba ya Yehova, adzalandira ulemerero waufumu ndipo adzalamulira pa mpando wake waufumu. Adzakhalanso wansembe pa mpando wake waufumu. Ndipo padzakhala mtendere.’
14 Chipewa cha ufumucho adzachipereka kwa Helemu, Tobiya, Yedaya, ndi kwa Heni mwana wa Zefaniya, kuti chikhale chikumbutso mʼNyumba ya Yehova.
15 Anthu okhala kutali adzabwera kudzathandiza kumanga Nyumba ya Yehova, ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. Zimenezi zidzachitika ngati mudzamvera mwachangu Yehova Mulungu wanu.”