3
Chiweruzo pa Yerusalemu ndi Yuda
1 Taonani tsopano, Ambuye
Yehova Wamphamvuzonse,
ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda
zinthu pamodzi ndi thandizo;
adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
2 anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,
oweruza ndi aneneri,
anthu olosera ndi akuluakulu,
3 atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,
aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
4 Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;
ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
5 Anthu adzazunzana,
munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.
Anthu wamba adzanyoza
akuluakulu.
6 Munthu adzagwira mʼbale wake
mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,
“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;
lamulira malo opasuka ano!”
7 Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,
“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.
Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;
musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
8 Yerusalemu akudzandira,
Yuda akugwa;
zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,
sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
9 Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;
amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;
salibisa tchimo lawolo.
Tsoka kwa iwo
odziputira okha mavuto.
10 Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,
pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
11 Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!
Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
12 Achinyamata akupondereza anthu anga,
ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.
Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;
akukuchotsani pa njira yanu.
13 Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;
wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
14 Yehova akuwazenga milandu
akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:
“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;
nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
15 Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,
nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”
Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
16 Yehova akunena kuti,
“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,
akuyenda atakweza makosi awo,
akukopa amuna ndi maso awo
akuyenda monyangʼama
akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
17 Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;
Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
18 Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi, 19 ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope, 20 maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa, 21 mphete ndi zipini, 22 zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama, 23 magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
24 Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,
mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;
mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;
mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;
mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
25 Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,
asilikali ako adzafera ku nkhondo.
26 Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;
Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.