2
Phiri la Yehova 
  1 Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:   
 2 Mʼmasiku otsiriza,  
phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa  
kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,  
lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,  
ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.   
 3 Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,  
“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,  
ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.  
Iye adzatiphunzitsa njira zake,  
ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”  
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,  
mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.   
 4 Iye adzaweruza pakati pa mayiko,  
ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.  
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu  
ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.  
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,  
kapena kuphunziranso za nkhondo.   
 5 Inu nyumba ya Yakobo, bwerani,  
tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.   
Tsiku la Yehova 
  6 Inu Yehova mwawakana anthu anu,  
nyumba ya Yakobo.  
Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa;  
amawombeza mawula ngati Afilisti,  
ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.   
 7 Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide;  
ndipo chuma chawo ndi chosatha.  
Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo;  
ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.   
 8 Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano;  
iwo amapembedza ntchito ya manja awo,  
amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.   
 9 Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa  
ndi kutsitsidwa.  
Inu Yehova musawakhululukire.   
 10 Lowani mʼmatanthwe,  
bisalani mʼmaenje,  
kuthawa kuopsa kwa Yehova  
ndi ulemerero wa ufumu wake!   
 11 Kudzikuza kwa anthu kudzatha,  
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa;  
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.   
 12 Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku  
limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama,  
ndipo adzagonjetsa  
onse amphamvu,   
 13 tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali,  
ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,   
 14 tsiku la mapiri onse ataliatali  
ndiponso la zitunda zonse zazitali,   
 15 tsiku la nsanja zonse zazitali  
ndiponso malinga onse olimba,   
 16 tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi  
ndiponso la mabwato onse okongola.   
 17 Kudzikuza kwa munthu kudzatha  
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa,  
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,   
 18 ndipo mafano onse adzatheratu.   
 19 Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe  
ndi mʼmaenje a nthaka,  
kuthawa mkwiyo wa Yehova,  
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,  
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.   
 20 Tsiku limenelo anthu adzatayira  
mfuko ndi mileme  
mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide,  
amene anawapanga kuti aziwapembedza.   
 21 Adzathawira mʼmapanga a matanthwe  
ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka  
kuthawa mkwiyo wa Yehova  
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,  
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.   
 22 Lekani kudalira munthu,  
amene moyo wake sukhalira kutha.  
Iye angathandize bwanji wina aliyense?