13
Lamba Womanga Mʼchiwuno 
  1 Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.”   2 Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.   
 3 Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti,   4 “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.”   5 Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.   
 6 Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.”   7 Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.   
 8 Pamenepo Yehova anandiwuza kuti,   9 “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu.   10 Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu.   11 Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.   
Zikopa Zothiramo Vinyo 
  12 “Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’   13 Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu.   14 Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”   
Yuda Adzapita ku Ukapolo 
  15 Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,  
musadzitukumule,  
pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.   
 16 Lemekezani Yehova Mulungu wanu  
asanagwetse mdima,  
mapazi anu asanayambe kupunthwa  
mʼchisisira chamʼmapiri.  
Asanasandutse kuwala  
mukuyembekezerako kukhala  
mdima wandiweyani.   
 17 Koma ngati simumvera,  
ndidzalira kwambiri  
chifukwa cha kunyada kwanu.  
Mʼmaso mwanga  
mwadzaza ndi misozi yowawa  
chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.   
 18 Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,  
“Tsikani pa mipando yaufumuyo,  
pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo  
zagwa pansi.”   
 19 Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa  
ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.  
Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,  
watengedwa yense ukapolo.   
 20 Tukula maso ako kuti uwone  
amene akubwera kuchokera kumpoto.  
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,  
nkhosa zanu zokongola zija?   
 21 Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira  
anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?  
Kodi sudzamva zowawa  
ngati za mayi pa nthawi yake yochira?   
 22 Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,  
“Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”  
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri  
kuti zovala zanu zingʼambike  
ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.   
 23 Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,  
kapena kambuku kusintha mawanga ake?  
Inunso amene munazolowera kuchita  
zoyipa simungathe kusintha.   
 24 “Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu  
amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.   
 25 Limeneli ndiye gawo lanu,  
chilango chimene ndakukonzerani  
chifukwa chondiyiwala Ine  
ndi kutumikira milungu yabodza,  
akutero Yehova.   
 26 Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso  
kuti umaliseche wanu uwonekere.   
 27 Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu  
ndi ziwerewere zanu,  
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.  
Tsoka iwe Yerusalemu!  
Udzakhala wosayeretsedwa  
pa zachipembedzo mpaka liti?”