14
Chilala, Njala, Lupanga 
  1 Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:   
 2 “Yuda akulira,  
mizinda yake ikuvutika;  
anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni,  
kulira kwa Yerusalemu kwakula.   
 3 Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.  
Apita ku zitsime  
osapezako madzi.  
Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi.  
Amanyazi ndi othedwa nzeru  
adziphimba kumaso.   
 4 Popeza pansi pawumiratu  
chifukwa kulibe madzi,  
alimi ali ndi manyazi  
ndipo amphimba nkhope zawo.   
 5 Ngakhale mbawala yayikazi  
ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo  
chifukwa kulibe msipu.   
 6 Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu  
nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe;  
maso awo achita chidima  
chifukwa chosowa msipu.”   
 7 Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,  
koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.  
Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu;  
ife takuchimwirani.   
 8 Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani  
ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso,  
chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno?  
Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?   
 9 Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,  
kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa?  
Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu,  
ndipo tikudziwika ndi dzina lanu;  
musatitaye ife!”   
 10 Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:  
“Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri;  
samatha kudziretsa.  
Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire,  
ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo  
ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”   
 11 Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.   12 Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”   
 13 Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”   
 14 Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo.   15 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala.   16 Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.   
 17 “Awuze mawu awa:  
“ ‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza  
usana ndi usiku;  
chifukwa anthu anga okondedwa  
apwetekeka kwambiri,  
akanthidwa kwambiri.   
 18 Ndikapita kuthengo,  
ndikuona amene aphedwa ndi lupanga;  
ndikapita mu mzinda,  
ndikuona amene asakazidwa ndi njala.  
Ngakhale aneneri pamodzi  
ndi ansembe onse atengedwa.’ ”   
 19 Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?  
Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni?  
Chifukwa chiyani mwatikantha chotere  
kuti sitingathenso kuchira?  
Ife tinayembekezera mtendere  
koma palibe chabwino chomwe chabwera,  
tinayembekezera kuchira  
koma panali kuopsezedwa kokhakokha.   
 20 Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu  
ndiponso kulakwa kwa makolo athu;  
ndithu ife tinakuchimwiranidi.   
 21 Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;  
musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero.  
Kumbukirani pangano lanu ndi ife  
ndipo musachiphwanye.   
 22 Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,  
kodi pali mulungu amene angagwetse mvula?  
Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu,  
popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu  
amene mukhoza kuchita zimenezi.