47
Uthenga Wonena za Afilisti 
  1 Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:   
 2 Yehova akuti,  
“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;  
adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.  
Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,  
mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.  
Anthu adzafuwula;  
anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira   
 3 akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,  
phokoso la magaleta ake  
ndi kulira kwa mikombero yake.  
Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;  
manja awo adzangoti khoba.   
 4 Pakuti tsiku lafika  
lowononga Afilisti onse  
ndi kupha onse otsala,  
onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.  
Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,  
otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.   
 5 Anthu a ku Gaza ameta mipala;  
anthu a ku Asikeloni akhala chete.  
Inu otsala a ku chigwa,  
mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?   
 6 “Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,  
kodi udzapumula liti?  
Bwerera mʼmalo ako;  
ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’   
 7 Koma lupangalo lidzapumula bwanji  
pamene Yehova walilamulira  
kuti lithire nkhondo  
Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”