48
Uthenga Wonena za Mowabu 
  1 Ponena za Mowabu:  
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,  
“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.  
Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;  
linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.   
 2 Palibenso amene akutamanda Mowabu;  
ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:  
‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’  
Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;  
ankhondo adzakupirikitsani.   
 3 Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.  
Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’   
 4 Mowabu wawonongeka;  
ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.   
 5 Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,  
akulira kwambiri pamene akupita.  
Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka  
pa njira yotsikira ku Horonaimu.   
 6 Thawani! Dzipulumutseni;  
khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.   
 7 Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,  
nanunso mudzatengedwa ukapolo,  
ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,  
pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.   
 8 Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,  
ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.  
Chigwa chidzasanduka bwinja  
ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa  
monga Yehova wayankhulira.   
 9 Mtsineni khutu Mowabu  
chifukwa adzasakazika;  
mizinda yake idzasanduka mabwinja,  
wopanda munthu wokhalamo.   
 10 “Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!  
Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!   
 11 “Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,  
ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,  
osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;  
iye sanatengedwepo ukapolo.  
Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja  
ndipo fungo lake silinasinthe.   
 12 Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”  
akutero Yehova,  
“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko  
ndipo adzamukhutula;  
adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake  
pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.   
 13 Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,  
monga momwe Aisraeli anachitira manyazi  
ndi Beteli amene ankamukhutulira.   
 14 “Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.  
Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’   
 15 Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;  
anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”  
ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.   
 16 Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;  
masautso ake akubwera posachedwa.   
 17 Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,  
inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;  
nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,  
taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”   
 18 “Tsikani pa ulemerero wanu  
ndipo khalani pansi powuma,  
inu anthu okhala ku Diboni,  
pakuti wowononga Mowabu  
wabwera kudzamenyana nanu,  
wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.   
 19 Inu amene mumakhala ku Aroeri,  
imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.  
Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,  
afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ”   
 20 Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.  
Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!  
Lengezani ku mtsinje wa Arinoni  
kuti Mowabu wawonongedwa.   
 21 Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,  
ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,   
 22 Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,   
 23 Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,   
 24 Keriyoti ndi Bozira  
ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.   
 25 Mphamvu za Mowabu zawonongeka;  
mkono wake wathyoka,”  
akutero Yehova.   
 26 “Muledzeretseni Mowabu,  
chifukwa anadzikuza powukira Yehova.  
Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;  
mulekeni akhale chinthu chomachiseka.   
 27 Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?  
Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba  
kuti nthawi zonse poyankhula za iye,  
iwe uzimupukusira mutu momunyoza?   
 28 Inu amene mumakhala ku Mowabu,  
siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.  
Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake  
pa khomo la phanga.   
 29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu,  
kunyada kwake nʼkwakukulu.  
Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.  
Ali ndi mtima wodzikweza.   
 30 Ine ndikuzidziwa ntchito zake,  
akutero Yehova.  
Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.   
 31 Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,  
ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,  
ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.   
 32 Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.  
Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa  
imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;  
zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.  
Wowononga wasakaza  
zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.   
 33 Chimwemwe ndi chisangalalo zatha  
ku minda ya zipatso ya ku Mowabu.  
Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;  
palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.  
Ngakhale kufuwula kulipo,  
koma sikufuwula kwa chimwemwe.   
 34 “A ku Hesiboni ndi Eleali akulira  
ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,  
kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.  
Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.   
 35 Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu  
kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera  
ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”  
akutero Yehova.   
 36 “Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.  
Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro  
chifukwa chuma chimene anachipata chatha.   
 37 Aliyense wameta mutu wake  
ndi ndevu zake;  
manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,  
ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.   
 38 Pa madenga onse a ku Mowabu  
ndiponso mʼmisewu yake  
anthu akungolira,  
pakuti ndaphwanya Mowabu  
ngati mtsuko wopanda ntchito,”  
akutero Yehova.   
 39 “Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!  
Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.  
Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,  
chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”   
 40 Yehova akuti,  
“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga  
chimene chatambalitsa mapiko ake.   
 41 Mizinda idzagwidwa  
ndipo malinga adzalandidwa.  
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu  
idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.   
 42 Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu  
chifukwa unadzikuza powukira Yehova.   
 43 Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira  
inu anthu a ku Mowabu,”  
akutero Yehova.   
 44 “Aliyense wothawa zoopsa  
adzagwera mʼdzenje,  
aliyense wotuluka mʼdzenje  
adzakodwa mu msampha.  
Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu  
pa nthawi ya chilango chake,”  
akutero Yehova.   
 45 “Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni  
chifukwa chotopa.  
Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,  
malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.  
Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,  
dziko la anthu onyada.   
 46 Tsoka kwa iwe Mowabu!  
Anthu opembedza Kemosi awonongeka.  
Ana ako aamuna ndi aakazi  
atengedwa ukapolo.   
 47 “Komabe masiku akutsogolo  
ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”  
akutero Yehova.  
Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.