2
Haa, Ambuye waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni
ndi mtambo wa mkwiyo wake!
Iye wataya pansi ulemerero wa Israeli
kuchoka kumwamba.
Pa tsiku la mkwiyo wake Iye sanakumbukirenso
popondapo mapazi ake.
 
Ambuye anawononga midzi yonse ya Yakobo mopanda chifundo;
mu mkwiyo wake anagwetsa
malinga a mwana wamkazi wa Yuda.
Anagwetsa pansi mochititsa manyazi
maufumu ndi akalonga ake.
 
Atakwiya kwambiri, Ambuye anathyola
nyanga iliyonse ya Israeli.
Anabweza dzanja lake lamanja
pamene mdani anamuyandikira.
Ambuye anatentha fuko la Yakobo ngati moto wonyeketsa
umene umawononga zinthu zonse zomwe zili pafupi.
 
Wakokera uta wake pa ife ngati ndife adani;
wayimiritsa dzanja lake pa ife ngati ndife adani,
ndipo anapha onse amene tinkawayangʼana monyadira.
Ukali wake ukuyaka ngati moto
pa tenti ya mwana wamkazi wa Ziyoni.
 
Ambuye ali ngati mdani;
wawonongeratu Israeli;
wawonongeratu nyumba zake zonse zaufumu
ndipo wawononga malinga ake.
Iye wachulukitsa kubuma ndi kulira
kwa mwana wamkazi wa Yuda.
 
Wagwetsa malo ake okhalamo ngati khumbi la mʼmunda;
wawononga malo ake a msonkhano.
Yehova wayiwalitsa Ziyoni
maphwando ake oyikika ndi masabata ake.
Mokwiya kwambiri, Iye ananyoza
mfumu ndi wansembe.
 
Ambuye wakana guwa lake la nsembe
ndipo wasiya malo ake opatulika.
Iye wapereka makoma a nyumba zake zaufumu
kwa mdani wake;
adaniwo anafuwula mʼnyumba ya Yehova
ngati kuti ndi pa tsiku la chikondwerero.
 
Yehova anatsimikiza kugwetsa
makoma a mwana wamkazi wa Ziyoni.
Anawayesa ndi chingwe
ndipo sanafune kuleka kuwagwetsa.
Analiritsa malinga ndi makoma;
onse anawonongeka pamodzi.
 
Zipata za Yerusalemu zalowa pansi;
wathyola ndi kuwononga mipiringidzo yake.
Mfumu ndi akalonga ake agwidwa ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
palibenso lamulo,
ndipo aneneri ake sakupeza
masomphenya kuchokera kwa Yehova.
 
10 Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni
akhala chete pansi;
awaza fumbi pa mitu yawo
ndipo avala ziguduli.
Anamwali a Yerusalemu
aweramitsa mitu yawo pansi.
 
11 Maso anga atopa ndi kulira,
ndazunzika mʼmoyo mwanga,
mtima wanga wadzaza ndi chisoni
chifukwa anthu anga akuwonongeka,
chifukwa ana ndi makanda akukomoka
mʼmisewu ya mu mzinda.
 
12 Anawo akufunsa amayi awo kuti,
“Kodi tirigu ndi vinyo zili kuti?”
pamene akukomoka ngati anthu olasidwa
mʼmisewu ya mʼmizinda,
pamene miyoyo yawo ikufowoka
mʼmanja mwa amayi awo.
 
13 Ndinganene chiyani za iwe?
Ndingakufanizire ndi chiyani,
iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?
Kodi ndingakufanizire ndi yani
kuti ndikutonthoze,
iwe namwali wa Ziyoni?
Chilonda chako ndi chozama ngati nyanja,
kodi ndani angakuchiritse?
 
14 Masomphenya a aneneri ako
anali abodza ndi achabechabe.
Iwo sanakupulumutse kuti usapite ku ukapolo
poyika poyera mphulupulu zako.
Mauthenga amene anakupatsa
anali achabechabe ndi osocheretsa.
 
15 Onse oyenda mʼnjira yako
akukuwombera mʼmanja;
akugwedeza mitu yawo ndi kukunyodola
iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu:
“Kodi mzinda uja ndi uwu umene unkatchedwa
wokongola kotheratu,
chimwemwe cha dziko lonse lapansi?”
 
16 Adani ako onse akutsekulira pakamwa ndi kukunyoza;
iwo akunyogodola ndi kukukuta mano awo,
ndipo akuti, “Tamumeza.
Tsiku ili ndi lomwe timayembekezera;
tili ndi moyo kuti tilione.”
 
17 Yehova wachita chimene anakonzeratu;
wakwaniritsa mawu ake,
amene anatsimikiza kale lomwe.
Wakuwononga mopanda chifundo,
walola mdani kuti akondwere chifukwa cha kugwa kwako,
wakweza mphamvu za adani ako.
 
18 Mitima ya anthu
ikufuwulira Ambuye.
Iwe khoma la mwana wamkazi wa Ziyoni,
misozi yako itsike ngati mtsinje
usana ndi usiku;
usadzipatse wekha mpumulo,
maso ako asaleke kukhetsa misozi.
 
19 Dzuka, fuwula usiku,
pamene alonda ayamba kulondera;
khuthula mtima wako ngati madzi
pamaso pa Ambuye.
Kweza manja ako kwa Iye
chifukwa cha miyoyo ya ana ako,
amene akukomoka ndi njala
mʼmisewu yonse ya mu mzinda.
 
20 Inu Yehova, onani, ndipo ganizirani:
kodi ndani amene mwamuchitirapo zinthu ngati izi?
Kodi amayi adye ana awo,
amene amawasamalira?
Kodi ansembe ndi aneneri awaphere
mʼmalo opatulika a Ambuye?
 
21 Anyamata ndi okalamba aligone pamodzi
pa fumbi la mʼmisewu ya mu mzinda;
anyamata anga ndi anamwali anga
aphedwa ndi lupanga.
Inu Yehova mwawapha pa tsiku la mkwiyo wanu;
mwawapha mopanda chifundo.
 
22 Ngati momwe mumayitanira pa tsiku la phwando,
chimodzimodzinso mwandiyitanira zoopsa mbali zonse.
Pa tsiku limene Yehova wakwiya
palibe amene angathawe ndi kukhala ndi moyo;
mdani wanga wawononga
onse amene ndinkawasamala ndi kuwalera.