3
Ine ndine munthu amene ndaona masautso
ndi ndodo ya ukali wake.
Wandipititsa kutali ndipo wandiyendetsa
mu mdima osati mʼkuwala;
zoonadi anandikantha ndi dzanja lake
mobwerezabwereza tsiku lonse.
 
Wakalambitsa khungu langa ndi mnofu wanga,
ndipo waphwanya mafupa anga.
Wandizinga ndi kundizungulira
ndi zowawa ndi zolemetsa.
Wandikhazika mu mdima
ngati amene anafa kale.
 
Wandimangira khoma kotero kuti sindingathawe,
wandimanga ndi maunyolo.
Ngakhale pamene ndifuwula kapena kupempha chithandizo,
amakana pemphero langa.
Wanditsekera njira yanga ndi miyala yosema;
ndipo wakhotetsa tinjira tanga.
 
10 Wandidikirira ngati chimbalangondo,
wandibisalira ngati mkango.
11 Wandikokera pambali ndi kundingʼambangʼamba,
ndipo wandisiya wopanda thandizo.
12 Wakoka uta wake
ndipo walunjikitsa mivi yake pa ine.
 
13 Walasa mtima wanga
ndi mivi ya mʼphodo mwake.
14 Ndinakhala choseketsa cha anthu anga onse;
amandinyodola mʼnyimbo zawo tsiku lonse.
15 Wandidyetsa zowawa
ndipo wandimwetsa ndulu.
 
16 Wathyola mano anga ndi miyala;
wandiviviniza mʼfumbi;
17 Wandichotsera mtendere;
ndayiwala kuti kupeza bwino nʼchiyani.
18 Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wachoka
ndi zonse zimene ndimayembekeza kwa Yehova.”
 
19 Kukumbukira masautso anga ndi kusowa pokhala,
zili ngati zowawa ndi ndulu.
20 Ine ndikuzikumbukira bwino izi,
ndipo moyo wanga wathedwa mʼkati mwanga.
21 Komabe ndimakumbukira zimenezi,
nʼchifukwa chake ndili ndi chiyembekezo.
 
22 Ife sitinawonongekeretu chifukwa chikondi cha Yehova ndi chachikulu,
ndi chifundo chake ndi chosatha.
23 Zimaoneka zatsopano mmawa uliwonse;
kukhulupirika kwanu nʼkwakukulu.
24 Mu mtima mwanga ndimati, “Yehova ndiye zanga zonse;
motero ndimamuyembekezera.”
 
25 Yehova ndi wabwino kwa amene amayembekezera Iye,
kwa munthu amene amafunafuna Iyeyo;
26 nʼkwabwino kudikira chipulumutso cha
Yehova modekha.
27 Nʼkwabwino kuti munthu asenze goli
pamene ali wamngʼono.
 
28 Akhale chete pa yekha,
chifukwa Yehova wamusenzetsa golilo.
29 Abise nkhope yake mʼfumbi
mwina chiyembekezo nʼkukhalapobe.
30 Apereke tsaya lake kwa iye amene angamumenye,
ndipo amuchititse manyazi.
 
31 Chifukwa Ambuye satayiratu
anthu nthawi zonse.
32 Ngakhale amabweretsa zowawa, Iye adzawachitira chifundo,
chifukwa chikondi chake ndi chosatha.
33 Pakuti sabweretsa masautso mwadala,
kapena zowawa kwa ana a anthu.
 
34 Kuphwanya ndi phazi
a mʼndende onse a mʼdziko,
35 kukaniza munthu ufulu wake
pamaso pa Wammwambamwamba,
36 kumana munthu chiweruzo cholungama—
kodi Ambuye saona zonsezi?
 
37 Kodi ndani angayankhule zinthu nʼkuchitika
ngati Ambuye sanavomereze?
38 Kodi zovuta ndi zabwino sizituluka
mʼkamwa mwa Wammwambamwamba?
39 Kodi nʼchifukwa chiyani munthu aliyense wamoyo amadandaula
akalangidwa chifukwa cha machimo ake?
 
40 Tiyeni tisanthule ndi kuyesa njira zathu,
ndipo tiyeni tibwerere kwa Yehova.
41 Tiyeni tikweze mitima yathu ndi manja athu
kwa Mulungu kumwamba ndipo tinene kuti:
42 “Ife tachimwa ndi kuwukira
ndipo inu simunakhululuke.
 
43 “Mwadzikuta ndi mkwiyo ndi kutilondola ndipo
mwatitha mopanda chifundo.
44 Mwadzikuta mu mtambo
kotero mapemphero athu sakukufikani.
45 Mwatisandutsa zinyatsi ndi zinyalala
pakati pa mitundu ya anthu.
 
46 “Adani anthu atitsekulira pakamwa.
47 Ife tadzazidwa ndi mantha pakuti tagwa mʼdzenje,
tapasuka ndi kuwonongedwa.”
48 Misozi mʼmaso mwanga ikungoti mbwembwembwe
chifukwa anthu anga akuwonongedwa.
 
49 Misozi idzatsika kosalekeza,
ndipo sidzasiya,
50 mpaka Yehova ayangʼane pansi
kuchokera kumwamba ndi kuona.
51 Mtima wanga ukupweteka poona zimenezi
chifukwa cha akazi onse a mu mzinda.
 
52 Akundisaka ngati mbalame,
amene anali adani anga, popanda chifukwa.
53 Ayesa kundipha pondiponya mʼdzenje
ndi kundiponya miyala;
54 madzi anamiza mutu wanga
ndipo ndinkaganiza kuti imfa yayandikira.
 
55 Ndinayitana dzina lanu Inu Yehova,
kuchokera mʼdzenje lozama.
56 Inu munamva kudandaula kwanga. “Mundimvere
kulira kwanga kopempha thandizo.”
57 Munafika pafupi pamene ndinakuyitanani,
ndipo munati, “Usaope.”
 
58 Inu Ambuye munandiwombola ku mlandu wanga;
munapulumutsa moyo wanga.
59 Yehova, mwaona zoyipa zimene andichitira.
Mundiweruzire ndinu!
60 Mwaona kuzama kwa kubwezera kwawo,
chiwembu chawo chonse pa ine.
 
61 Inu Yehova mwamva kunyoza kwawo,
chiwembu chawo chonse pa ine,
62 manongʼonongʼo a adani anga
ondiwukira ine tsiku lonse.
63 Tawaonani! Kaya ali pansi kapena kuyimirira,
akundinyoza mu nyimbo zawo.
 
64 Inu Yehova, muwabwezere chowayenera,
chifukwa cha zimene manja awo achita.
65 Phimbani mitima yawo,
ndipo matemberero anu akhale pa iwo!
66 Muwalondole mwaukali ndipo
muwawonongeretu pa dziko lapansi.