7
Iwe namwali waufumu, mapazi ako ngokongola
mu nsapato wavalazo!
Ntchafu zako nʼzowumbika bwino ngati miyala yamtengowapatali,
ntchito ya manja ya mmisiri waluso.
Mchombo wako uli ngati chikho chowumbika bwino
chimene nthawi zonse ndi chodzaza ndi vinyo.
Chiwuno chako ndi choningʼa ngati mtolo wa tirigu
utazunguliridwa ndi maluwa okongola.
Mawere ako akuoneka ngati ana awiri a mbawala,
ngati mphoyo zamapasa.
Khosi lako lili see! ngati nsanja ya mnyanga wa njovu.
Maso ako ali ngati mayiwe a ku Hesiboni,
amene ali pafupi ndi chipata cha Bati Rabimu.
Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni,
yoyangʼana ku Damasiko.
Mutu wako uli bwinobwino nengʼaa ngati phiri la Karimeli.
Tsitsi lako lili ngati nsalu yakuda yaufumu;
mfumu yakopeka ndi maonekedwe ake okongola.
Ndiwe wokongola kwambiri ndiponso wosangalatsa,
iwe wokondedwa, namwali wokondweretsawe!
Msinkhu wako uli ngati mtengo wa mgwalangwa,
ndipo mawere ako ali ngati phava la zipatso.
Ndinati, “Ndikwera mtengo wa mgwalangwa;
ndidzathyola zipatso zake.”
Mawere ako ali ngati maphava a mphesa,
fungo la mpweya wako lili ngati ma apulosi,
ndipo pakamwa pako pali ngati vinyo wokoma kwambiri.
Mkazi
Tsono vinyo ameneyu amuthirire wachikondi wanga,
ayenderere bwino pa milomo yake ndi mano ake.
10 Wokondedwayo ine ndine wake,
ndipo chilakolako chake chili pa ine.
11 Bwera wachikondi wanga, tiye tipite ku madera a ku midzi,
tikagone ku midzi.
12 Tiye tilawirire mmamawa kupita ku minda ya mpesa,
tikaone ngati mitengo ya mpesa yayamba kuphukira,
ngati maluwa ake ayamba kuoneka,
komanso ngati makangadza ayamba kuonetsa maluwa.
Kumeneko ndidzakuonetsa chikondi changa.
13 Mitengo ya mankhwala a chisulo ikupereka fungo lake labwino,
ndipo pa khomo pathu pali zipatso zonse zokoma,
zatsopano ndi zakale zomwe,
zimene ndakusungira wokondedwa wanga.